07/09/2023
*Kambe Herbal Healthcare Clinic*
+265 888 394 309
*_ZOYENERA KUDZIWA PA UMOYO WABWINO._*
👁️ *_Ndiye Poti Takhala Tikuchita Zimenezi Mosadziwa, Tsopano Ndi Nthawi Yabwino Yoti Timwe Kambe herbal detox Juice Remedy_*
✍🏾 *Pali zinthu zambiri zotibweretsera mabvuto pa umoyo wathu mosadziwa. Zotsatirazi ndi zina za zomwe tiyenera kuchepetsa,kapena kungosiiratu.*
1. Musamatenthetsenso mafuta, kapena kugwiritsanso ntchito mafuta omwe agwira kale ntchito. Mafuta otenthetsedwanso amasanduka phalaphala lomwe limapangitsa magazi kuvutika kuyenda mthupi lathu.
2. Musamwe madzi panthawi imene mukudya. Chizolowezi ichi sichabwino. Chimapangitsa kuti thupi lisamagaye bwino chakudya, komanso kuchulutsa mpweya oipa mmimba mwathu.
3. Musamwe madzi ozizira kwambiri mukangodya kumene chifukwa amakapangitsa mafuta omwe mwadya kuyamba kuundana. Mmalomwake, muzimwa madzi otentha kuti azikasungunula ndi kutsuka mafutawa.
4. Chepetsani kapena siilanitu kudya zakudya za mafuta kwambiri komanso zomwe zimapangitsa magazi kulimba. Zakudya izi ndi ngati Chips, nkhuku ndi nyama zina zokazinga komanso zina zotere. Zakudya izi ndi zimene mochulukira zimapangitsa mavuto a mtima, kunenepa kwambiri, mavuto a chiwindi komanso matenda ena.
5. Chepetsani kapena siilanitu kudya nyama yofiira monga ya ng'ombe, ndi zina zotere.
Nyama ya ng'ombe imachedwa kugaika poyerekeza ndi nyama zina monga nkhuku ndi nkhumba. Nyama yofiira ikakhalitsa mthupi, imatambitsa acid wa mu mkodzo, yemwe amaononga khungu la matumbo athu zomwe zimayambitsa matenda a ma ulcers. Palinso mavuto ena omwe amayambika nyama yofiira monga gout, cancer ndi zina zambiri.
6. Imwani madzi mphindi 30 kapena 40 musanadye, kapena mutamaliza kudya. Izi zimathandiza kuti thupi lathu ligaye bwino chakudya.
7. Idya zipatso musanadye chakudya champhamvu, osati mukamaliza kudya.
Izi ndi zipatso makamaka zomwe timadya ndi makoko omwe ngati magwafa, mango, mapichesi ndi zina zotere. Zipatso izi zimatenga mphindi 30 zokha kuti zigayike.