28/04/2025
*ALOE VERA / ALUVERA*
Awa ndi maluwa amene anthu amadzala komanso zimakonda kumera mmbali mwa madzi. Duwa lake limakhala lobiliwira laminga mmbalimu.
Dzina la aluvera Linachokera ku Arabic "alloeh" kutanthauza kuti duwa lowala lowawa.
*UBWINO WAKE WA MALUWA A ALUVERA*
✓ Mukapaka/kudzola madzi ake aja pa khungu lanu zilonda za pakhungu zimatha (acne) komanso totupa ta pakhungu kapena mkamwa (rash) timatha.
✓ Aluvera amathandizira kuchilitsa mabala.
✓Aluvera amathandizilanso kuti mlingo wa sugar usakwere mnthupi.
✓ Aluvera amathandiza kutsuka m'magazi komanso m'matumbo (detoxification)
✓ Kuthandizira kugaya chakudya.
✓ Aluvera Ali ndi maantibiotic amene amathana ndi infection yomwe imayambitsidwa kamba ka ma bacteria.
✓Aluvera amathananso ndi nthenda ya UTI.
✓Aluvera amachotsa ziphuphu kumanso.
✓Aluvera amachedwetsa kukalamba (anti aging)
✓✓ Mukadzimbidwa thamangirani Pali aluvera ikani mapisi mmadzi then kumwa madzi akewo
✓✓ M***a kumwa aluvera poduladula tizidutswa nkuika mmadzi olo mu botolo nkumamwa madzi akewo kapena kuwilitsa mapisiwo Kwa mphindi khumi then nkumwa madzi akewo, m***a kuyikamo uchi wa chilengedwe mukafuna.
✓✓ Kumwa madzi a aluvera mmawa musanadye kalikonse kumathandiza kuchepetsa thupi, chisamaliro Cha nkamwa/dental komanso kuBIBA mosavutikira.
✓✓ Kwa Iwo amene kumalo awo obisika kuli kwakuda kapena dark spots, tengani zankati mwa aluvera zija olo ngambani aluvera pakati nkumapakati Malo okudawo ndi aluvera uja Kwa 20-30 minutes.
✓✓ Tengani za mkati mwa aluvera ndikupaka ku nkhope kwanu usiku ndipo mudzathana ndi ziphuphu, blackspots komanso nkhope imasalala.
*NB: Kudya chakudya chilichonse mopyoza mlingo wake kumabweretsa mavuto.*