Vision Dental Clinic

Vision Dental Clinic Affordable dental services

Have you visited your dentist for check up this year?Remember prevention is better and cheaper than cure.
22/10/2024

Have you visited your dentist for check up this year?Remember prevention is better and cheaper than cure.

29/06/2024

Kodi ndi garage iti kumene amamata ma crack a windscreen?

02/05/2023

Remember to visit your nearest dental clinic for check up before its too late

02/05/2023
25/12/2022

Feeling Christmatic

14/10/2022

Masana ano ndikufuna tikambirane kuti ndi chifukwa chani anthu ena amamva kuwawa pochotsa dzino ngakhale atabaidwa mankhwala opangisa dzazi.
Poyamba tikumbusane kuti dzino silibooka tsiku limodzi mkuyamba kuwawa tsiku lomwelo, dzino limabooka pang'ono pang'ono ndipo limatenga miyezi ngakhale chaka kuti liyambe kuwawa,
Dzino liri ndi zigawo kapena kuti ma layer atatu,
Enamel _ gawo limeneli likabooka siliwawa

Dentine_ gawo limeneli likabooka limazizira mukamwa madzi kapena tea komanso kuwawa pakalowa chakudya; dzino lotere likamatidwa limakhala bwino bwino
Pulp __gawo ili ndi mmene mumakhala misempha ya dzino ndipo kuwola kwa dzino kukafika gawo ili misempha imatupa ndi kuyamba kuwawa kosowesa mtendere usana ndi usiku. Apa ndi pamene munthu amaganiza zopita ku chipatala kuti akachotsese dzino.
Chifukwa choti misempha yatupa nthawi dzina kumapeto kwa dzino kumayamba kupangika mafinya kapena kathuza.
Mukabaidwa mankhwala opangisa dzazi mankhwalawa amayenda ndi kuzizilisa misempha yonse yozungulira dzino lomwe likufuna kuchotsedwa koma mafinya amapanga block mankhwala kuti asafike mbali ina ya dzino ndipo zimenezi zimapangisa kuti dzino lizimvekabe kuwawa pochotsa ngakhale litabaidwa mankhwala ochuluka ,vuto ili likapitilira pamafunika kukamwa kaye ma antibiotics kuti mafinya aja athe komanso misempha isakhale yotupa, akatha ma antibiotics dzino limachoka bwino bwino popanda kuwawa kulikonse.
Zikomo

08/10/2022

Moni wa madzulo kwa nonse, ndipepese kwa onse amene munasiya kubwera ku clinic chifukwa msewu siunali bwino, pano unakonzedwa ndipo uli ndi tar, kuchokera pa Gulaye ku area 25c kwezekani mtunda straight kupita ku sector 3,mukamaliza mtunda muyan'gane kumanzere muona Vision Dental clinic
Zikomo

26/07/2021

Good evening to our valued clients, it looks some of you have difficulties to reach our clinic, the clinic is in Lilongwe area 25c, from Kanengo second turn right opposite Simsol filling station, you go straight with the road until the end of tarmac, you will see the clinic to your left. From area 49 second turn left opposite simsol filling station, you go straight with the road until the end of the tarmac, you will find us, good night and remember to brush your teeth before going to sleep.

29/03/2021

Mswachi wabwino ndi umene ma brush ake ndi ofewa komanso ali straight, mswachi ukuyenera kusinthidwa ngati ma brush agona chifukwa sungathenso kutsuka mano moyenera. Mswachi womwe ma brush ake ndi olimba umapala mano ndi ma gum ndipo mtsogolo mano amayamba kuzizira .Dziwani kuti mswachi sumachoza zakudya zonse choncho ndi kofunika kupita ku chipatala miyezi six ili yonse kukatsukisa mano omwe sangayere ndi mswachi.

22/03/2021
25/01/2021

Moni nonse mchaka ichi chatsopano,lero tikambirana za dzino lotupa, chomwe chimachitika ndi choti ma bacteria amalowa mu dzino kukafika mu fupa kenako ndi kukafika mu tsaya kapena khungu, nthawi zina ma bacteria amalowa mu msempha wa magazi ndi kukafika ku mtima, akafika ku mtima umayamba kutupa ndipo ngati munthu analandira thandizo mwansanga akhoza kufa kumene.Choncho popewa izi tizithamangira ku chipatala Ngati dzino likuwawa osati kuikapo petrol ,garlic ndi zisamba. Ku chipatala timapeleka mankhwala kuti tizilombo tija tife kenako kuchotsa dzino patatha sabata imodzi .mukhake ndi tsiku lopambana

Address

Chiuzimbi
Lilongwe

Opening Hours

Monday 08:00 - 17:00
Tuesday 08:00 - 17:00
Wednesday 08:00 - 17:00
Thursday 08:00 - 17:00
Friday 08:00 - 17:00
Sunday 08:00 - 17:00

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Vision Dental Clinic posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Share on Facebook Share on Twitter Share on LinkedIn
Share on Pinterest Share on Reddit Share via Email
Share on WhatsApp Share on Instagram Share on Telegram