Chipatala Cha Mawanja

Chipatala Cha Mawanja Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Chipatala Cha Mawanja, Marriage Therapist, 227 main road, Cape Town Southern Suburbs.
(5)

KODI NDI MAMUNA UTI AMENE AMAVUTIKA KWAMBIRI?Mwamuna amene amavutika kwambiri si uja amene ali ndi chuma chochepa, koma ...
23/04/2026

KODI NDI MAMUNA UTI AMENE AMAVUTIKA KWAMBIRI?

Mwamuna amene amavutika kwambiri si uja amene ali ndi chuma chochepa, koma uja amene samamvera malangizo a mkazi wake.

• Kugwiritsa ntchito maganizo oti mkazi wako amalankhula kwambiri, pamene kwenikweni akungokusamalira.
• Kuganiza kuti mkazi wako akufuna kukulamulira, pamene zoona zake akufuna kukuteteza.
• Kumva ngati malangizo a mkazi wako akuchepetsa ulemu wako, pamene mkaziyo ndi amene amasunga bata ndi kulinganiza moyo wako.

Mkazi amadziwa nthawi imene mwamuna wake ayenera kuima ndi kupuma, komanso nthawi imene ayenera kulimbikitsidwa kupita patsogolo.
Chifukwa mkazi ndiye amadziwa kutopa, ululu, ndi mmene mwamuna wake akumvera.

Mwamuna amene amavutika kwambiri nthawi zambiri amanyalanyaza chenjezo, madalitso, ndi chitetezo chimene chili mu mtima wa mkazi wake womvera ndi wodzichepetsa.

AZIBAMBO INU ZIMVERANI MAGANIZO AZIKAZI ANU...
nthawi zambiri amakufunilani zabwino...

MUNTHU WABAMBO AKAMAMVEREDWA NDI MKAZI WAKE AMAKHALA NGATI CHITSIRU KWA AKAZI ENATsiku lina kuntchito, mzimai wina wake ...
23/04/2026

MUNTHU WABAMBO AKAMAMVEREDWA NDI MKAZI WAKE AMAKHALA NGATI CHITSIRU KWA AKAZI ENA

Tsiku lina kuntchito, mzimai wina wake yemwe amagwira limodzi ndi bambo wina Ku ntchito anauza mwamuna wokwatiwa kuti:

“Ukudziwa… ukadakhala single, ndikanakukonda ndikukusamalira bwino.”
Mwamunayo anangoseka pang’ono.

Mkazi uja anawonjezera kuti:
“Mkazi wako ali ndi mwayi. Koma m***a mtima… ndikuganiza kuti ine ndingakusamalire bwino kuposa iye.”

Mwamunayo anamuyang’ana n’kunena mwakachetechete:
“Mkazi wanga si amene ali ndi mwayi.”
Mkazi uja anadabwa n’kufunsa kuti:
“Ukutanthauza chiyani?”
Mwamunayo anamwetulira n’kunena kuti:
“Wamwayi ndi ine.
Ndipo sindine wopusa moti ndingataye zimene ndili nazo.”

Pambuyo pake mkazi uja angoti zyoli pansi,kusowa choyankhula.

Nthawi zina, kukhulupirika kumangokhala mwamuna kapena mkazi amene amakumbukira bwino zimene ali nazo kale.

23/04/2026

Ena sadzakhala ndi banja lopambana, komanso sadzachita bwino pa nkhani ya ndalama (sadzalemera) , chifukwa cha anzawo amene amasankha kukhala nawo.

Amzanu ena ndi oipa sakufunilani zabwino....

23/04/2026

Banja Lili lonse imafika nthawi yoti
Umadzifunsa wekha Kuti ,

Koma ineyo ndidamuloleranji uyu....

Si nokhayi ndi tonse,
Osagwa mphwayi tiyeni chitsogolo be...
Ameneyo ndi Mwamuna/mkazi wanu
Yemwe uja....

“CHIMENECHI NDI CHIFUKWA CHAKE MAMUNA AYENERA KUKHALA WOONA MTIMA KWA MKAZI WAKE”Amuna inu abale dziwani izi;- Chimene m...
22/04/2026

“CHIMENECHI NDI CHIFUKWA CHAKE MAMUNA AYENERA KUKHALA WOONA MTIMA KWA MKAZI WAKE”

Amuna inu abale dziwani izi;

- Chimene mkazi amaopa kwambiri si zolakwa zako—koma mabodza ako.

- Mkazi amatha kuyima nawe mu nyengo zovuta.
Amakhale woleza mtima pamene ukukalimbikira kupeza njira zoti zinthu zikuthekere.
Koma ukangoyamba kunama…
pamenepo chikhulupiriro chake pa iwe chimayamba kusweka pang’onopang’ono.

Chifukwa kwa mkazi, kuwona mtima si mawu okha—ndi chitetezo.

Ukakhala woona mtima, iye amamva kuti ali wofunika.

Amamva kuti akuphatikizidwa pa moyo wako.

- Koma ukamanama…
si nkhani yokha imene imasweka—
mtima wake umapwetekanso.

-Ndipo kukonzanso chikhulupirirocho
nkovuta kwambiri kuposa kuchisunga.

AZIBAMBO UMU NDI MMENE MUNGAKONDERERE MKAZI WANU1- Yambani tsiku ndi kumukumbatira ndi kumupsompsona, musanayambe ntchit...
22/04/2026

AZIBAMBO UMU NDI MMENE MUNGAKONDERERE MKAZI WANU

1- Yambani tsiku ndi kumukumbatira ndi kumupsompsona, musanayambe ntchito za tsikulo.

2- Muuzeni kuti “ndimakukonda” tsiku lililonse, osati pamene zinthu zikuyenda bwino zokha.

3- Musachoke kunyumba popanda kumupsompsona—ndi njira yosavuta yosonyeza kuti ndi wofunika kwa inu.

4- Mufunseni mmene alili pa tsiku, kungoti muwone mmene akuyendera(mutha kuyimba call or watsap msg).

5- Mukafika kunyumba, mumulandire ndi kukumbatira, kumupsompsona, komanso kumupatsa chidwi chenicheni.

6- Sonyezani chikondi kudzera mu zinthu zing’onozing’ono, kuphatikizapo kumuthandiza pa ntchito za m’nyumba.

7- Tsekani tsiku ndi kukumbatira ndi kumupsompsona musanagone—bweretsani mtendere ku mtima wake, osati kungokwaniritsa thupi lanu lokha.

ABALE TAMVETSERANI Ngakhale anthu ambiri amanena kuti, “Makolo athu sanasiyane/banja silidathe, banja lawo adaliyendetsa...
22/04/2026

ABALE TAMVETSERANI

Ngakhale anthu ambiri amanena kuti, “Makolo athu sanasiyane/banja silidathe, banja lawo adaliyendetsa bwino kuposa ife,” chowonadi chomvetsa chisoni ndi chakuti ambiri ankangokhala m’banja koma osakhala osangalala kwenikweni.

Kwa ambiri, banja linali longotsatira chikhalidwe, osati kufunafuna chimwemwe ndi mgwirizano weniweni.

Ena anapitiriza kukhala m’banja chifukwa analibe njira ina, makamaka chifukwa cha kusowa kwa ndalama kapena mavuto a moyo.

Kuphatikiza apo, nkhani ya kumvetsetsana maganizo (emotional intelligence) sinkalankhulidwa kwambiri.

Banja linali ngati ntchito yokakamiza, yopanda kulumikizana kwa maganizo mozama.

Kuuza m’badwo wamakono kuti ukhale ndi banja monga momwe makolo athu ankachitira sikungagwire ntchito kweni kweni.

M’badwo wamakono uyenera kupatsidwa zida ndi maphunziro okhudza mmene angamangire mabanja athanzi, osati kungokhala mu banja kokha basi.

Mfundo yayikulu ndi yakuti “mabanja athanzi.”mabanja achimwemwe

Ngakhale lero lino, ambiri ali m’mabanja akufa;
Palibe kulumikizana, amangokhala limodzi chifukwa cha ana kapena kugonana basi.

Banja lathanzi limamangidwa ndi kulankhulana kwabwino, kumvetsetsana bwino kwa maganizo, komanso kusamalira zosowa zosiyanasiyana za mwamuna ndi mkazi.

Anthu onse awiri ayenera kukhala okhutira komanso osangalala mu banja.

Ndi zomwe Ife a Chipatala Cha Mawanja timakhumbira aliyense atakhala nazo mu banja Lake....

22/04/2026

We choose US Everyday...

AZIBAMBO TAMVETSERANI Mukamakangana ndi mkazi wanu, kumbukirani zinthu zitatu izi:1- Musalole mkazi wanu kukhala ndi nja...
22/04/2026

AZIBAMBO TAMVETSERANI

Mukamakangana ndi mkazi wanu, kumbukirani zinthu zitatu izi:

1- Musalole mkazi wanu kukhala ndi njala.
Ngakhale muli okwiya, musamulole pa khomo panu pasowe chakudya.
Nthawi zambiri mkazi amapitiriza kuphika ndi kusamalira nyumba, ngakhale mtima wake ukupweteka.

2- Musamumenye kumaso umenewo ndi ufiti.
Nkhope ya mkazi ndi ulemu wake.

3- Mukamunyoza kapena kumuchitira nkhanza, chilonda chake chimakhala mumtima wake kwa nthawi yayitali/zimamuvuta kuyiwala.
Musamunyoze kapena kumuchepetsa/kumuyang'anila pansi.

Kumbukirani kuti ndi mkazi yemwe munasankha kukhala naye pa moyo wanu Onse,ndipo mudasankha nokha.

Kumbukirani: Mkazi amene mumamupweteka lero ndi yemweyo amene tsiku ndi tsiku amalimbana kuti ateteze nyumba yanu ndi banja lanu.
Mlemekezeni mkazi wanu....

AZIMAI SIYANI KUMUIMBA MLANDU MAMUNA WANU NTHAWI ZONSE-Ngati simukufuna kudzikonza nokha, musamamuone  mwamuna wanu ngat...
21/04/2026

AZIMAI SIYANI KUMUIMBA MLANDU MAMUNA WANU NTHAWI ZONSE

-Ngati simukufuna kudzikonza nokha, musamamuone mwamuna wanu ngati ndiye amene Ali vuto.

-Mumadzudzula utsogoleri wake, koma simufuna kuziona nokha Kuti mukusowa ulemu pa iyeyo.

-Mumadandaula kuti ali kutali ndi inu pa maganizo, koma mumanyalanyaza makoma amene inu munamangapo poyamba/mudatseka makoma onse..

Mwamuna si dokotala wa maganizo amene wapatsidwa ntchito yokonza mabala amene inu munasankha kunyalanyaza.
Iye sanakwatire inu kuti azinyamula katundu wa maganizo anu osachira.
Musamayembekezere kusamalidwa ngati mfumu pamene khalidwe lanu likusonyeza kudzikweza osati kukhulupirika.
Ukwati suwonongeka chifukwa cha munthu mmodzi yekha.
Umawonongeka pamene udindo (accountability) ukusowa.

MWAMUNA WODZIKONDERA KWAMBIRI NDI UYU:*Mwamuna amene amafuna banja lla  mtendere, koma iye mwini samabweretsa mtendere m...
21/04/2026

MWAMUNA WODZIKONDERA KWAMBIRI NDI UYU:

*Mwamuna amene amafuna banja lla mtendere, koma iye mwini samabweretsa mtendere mu mtima wa mkazi wake.

*Mwamuna amene amafuna kumvetsedwa, koma yekha sakufuna kumvetsa Za anzake.

*Mwamuna amene amaganiza kuti kukhala chete (kusayankhula) Kwa mkazi kumatanthauza kuti zonse zili bwino.

Koma choonadi ndi chakuti: nthawi zina kukhala chete zimangotanthauza kuti mkazi watopa ndi kufotokoza Za ululu wake kwa mwamuna amene samamumvera.

Ndiye amaongowona Kuti ndibwino ndingokhala chete.....

AZIMAI NDI AZIBAMBO TAMVERANI AZIBAMBO,Pakati pa makolo ako ndi mkazi wako, mkazi wako ndiye ayenera kubwera patsogolo,M...
21/04/2026

AZIMAI NDI AZIBAMBO TAMVERANI

AZIBAMBO,
Pakati pa makolo ako ndi mkazi wako, mkazi wako ndiye ayenera kubwera patsogolo,Mkazi wako Ndiye number 1!

AZIMAI,
Pakati pa mwamuna wako ndi makolo ako, mwamuna wako ndiye ayenera kubwera patsogolo,Mamuna WAKO Ndiye number 1!

Mukangokwatirana, awirinu mumakhala mmodzi.

Wokondedwa wako ndiye iweyo.

Palibe amene amayenera kubwera patsogolo kuposa iwe. Musamayambitse mikangano mu comment section.
Mudzingomvera...

Address

227 Main Road
Cape Town Southern Suburbs
7800

Telephone

+27685885545

Website

Services

Specialties

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chipatala Cha Mawanja posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Practice

Send a message to Chipatala Cha Mawanja:

Share